Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Pemphero la Davide.
17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
2 Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
maso anu aone chimene ndi cholungama.
3 Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
4 Kunena za ntchito za anthu,
monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
posatsata njira zachiwawa.
5 Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
mapazi anga sanaterereke.
6 Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
7 Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
8 Mundisunge ine ngati mwanadiso;
mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
9 kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.
Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.
Mawu Oyamba
1 Mʼdziko la Uzi munali munthu wina, dzina lake Yobu. Munthu ameneyu anali wosalakwa ndi wolungama mtima, ankaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. 2 Anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu, 3 ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa.
4 Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthanasinthana mʼnyumba zawo, ndipo ankayitana alongo awo atatu aja kudzadya ndi kumwa nawo. 5 Masiku aphwandowo atatha, Yobu ankawayitana kuti adzawayeretse. Mmamawa iye ankapereka nsembe yopsereza kuperekera mwana aliyense, poganiza kuti, “Mwina ana anga achimwa ndi kutukwana Mulungu mʼmitima yawo.” Umu ndi mmene Yobu ankachitira nthawi zonse.
Yobu Ayesedwa Koyamba
6 Ana a Mulungu atabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anafika nawo limodzi. 7 Yehova anati kwa Satanayo, “Kodi iwe ukuchokera kuti?”
Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”
8 Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa.”
9 Satana anayankha kuti, “Kodi Yobu amaopa Mulungu popanda chifukwa?” 10 “Kodi Inu simumamuteteza iyeyo, nyumba yake ndi zonse zimene ali nazo? Mwadalitsa ntchito ya manja ake, kotero kuti nkhosa ndi ngʼombe zake zili ponseponse mʼdzikomo. 11 Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kukantha zonse ali nazo ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.”
12 Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, tsono zonse zimene ali nazo ndaziyika mʼmanja mwako, koma iye yekhayo usamukhudze.”
Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova.
13 Tsiku lina pamene ana aamuna ndi ana aakazi a Yobu ankachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba mwa mkulu wawo, 14 wamthenga anabwera kwa Yobu ndipo anati, “Ngʼombe zanu zotipula ndipo abulu anu amadya chapafupi pomwepo, 15 tsono panabwera Aseba kudzatithira nkhondo ndi kutenga zonse. Apha antchito ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
16 Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Kunagwa mphenzi ndipo yapsereza nkhosa ndi antchito anu onse, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
17 Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Akasidi anadzigawa mʼmagulu atatu ankhondo ndipo anafika pa ngamira zanu ndi kuzitenga. Apha antchito anu onse ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
18 Iyeyo akuyankhulabe, panafikanso wamthenga wina nati, “Ana anu aamuna ndi aakazi amachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba ya mkulu wawo, 19 mwadzidzidzi chinayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nʼkudzawomba nyumba mbali zonse zinayi. Nyumbayo yawagwera ndipo afa, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
20 Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, 21 nati,
“Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga,
namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche.
Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga;
litamandike dzina la Yehova.”
22 Mu zonsezi, Yobu sanachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”
Za Kukhala Tcheru
34 “Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. 35 Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. 36 Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37 Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse. 38 Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.
Yudasi Avomera Kumupereka Yesu
22 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, 2 akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. 3 Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. 4 Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. 5 Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. 6 Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.