Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Zipatso Zoyamba ndi Chakhumi
26 Mukalowa ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, 2 mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake 3 ndipo mudzamuwuze wansembe amene ali pa ntchito pa nthawiyo kuti, “Ndikunenetsa lero kwa Yehova Mulungu wanu kuti ndabwera ku dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa ife.” 4 Wansembe adzatenga dengulo mʼmanja mwanu ndi kuliyika pansi patsogolo pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 5 Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka. 6 Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga. 7 Kenaka tinafuwulira Yehova, Mulungu wa makolo athu ndipo Yehova anamva mawu athu ndi kuona kusauka, kuvutika ndi kuponderezedwa kwathu. 8 Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa. 9 Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. 10 Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake. 11 Ndipo inu ndi Alevi pamodzi ndi alendo okhala pakati panu mudzakondwera mʼzinthu zonse zabwino zimene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, inu ndi a pa banja panu.
91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
2 Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
Mulungu wanga amene ndimadalira.”
9 Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo;
wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
10 Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera,
zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
11 Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,
kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;
12 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
13 Udzapondaponda mkango ndi njoka,
udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.
14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
ndidzakhala naye pa mavuto,
ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
ndi kumupulumutsa.”
8 Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira, 9 kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. 11 Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” 12 Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye 13 pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
Kuyesedwa kwa Yesu
4 Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu, 2 kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.
3 Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”
5 Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi. 6 Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna. 7 Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”
8 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
9 Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. 10 Pakuti kwalembedwa,
“Adzalamulira angelo ake za iwe
kuti akutchinjirize mosamala;
11 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
12 Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
13 Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.