Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 38

Salimo la Davide. Kupempha.

38 Yehova musandidzudzule mutapsa mtima
    kapena kundilanga muli ndi ukali.
Pakuti mivi yanu yandilasa,
    ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa;
    mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
Kulakwa kwanga kwandipsinja
    ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.

Mabala anga akuwola ndipo akununkha
    chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri;
    tsiku lonse ndimangolira.
Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika,
    mulibe thanzi mʼthupi langa.
Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu;
    ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.

Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,
    kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
10 Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha;
    ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga;
    anansi anga akhala kutali nane.
12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo,
    oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga;
    tsiku lonse amakonza zachinyengo.

13 Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve,
    monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
14 Ndakhala ngati munthu amene samva,
    amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
15 Ndikudikira Inu Yehova;
    mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere
    kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”

17 Pakuti ndili pafupi kugwa,
    ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
18 Ndikuvomereza mphulupulu zanga;
    ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
19 Ambiri ndi adani anga amphamvu;
    amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino
    amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

21 Inu Yehova, musanditaye;
    musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
22 Bwerani msanga kudzandithandiza,
    Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.

Levitiko 5:1-13

“ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa.

“ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa.

“ ‘Munthu akakhudza choyipitsa munthu cha mtundu uliwonse, ndipo pochikhudzapo ndi kuyipitsidwa nacho mosadziwa, munthuyo adzakhala wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.

“ ‘Munthu akalumbira mofulumira kapena mosasamala kuti adzachita chinthu, choyipa kapena chabwino, ngakhale kuti wachita izi mosadziwa kuti nʼkulakwa, pamene wazindira kulakwa kwake, iye adzakhalabe wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.

“ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo. Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo.

“ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. Tsono abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame imodzi ngati yopepesera tchimo. Apotole khosi koma osayidula mutu, kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 10 Pambuyo pake wansembe apereke mbalame inayo kuti ikhale chopereka chopsereza potsata mwambo wake. Wansembe atatha kupereka nsembe yopepesera tchimo limene munthu uja wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.

11 “ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. 12 Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 13 Umu ndi mmene wansembe adzachitire mwambo wopepesera machimo ena aliwonse amene munthu wachita, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Zopereka zonse zotsala zidzakhala za wansembeyo monga momwe amachitira ndi chopereka chachakudya.’ ”

Luka 17:1-4

Za Uchimo, Chikhulupiriro ndi Ntchito

17 Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa. Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha.

“Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni. Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.