Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
120 Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga,
ndipo Iye amandiyankha.
2 Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,
ndi kwa anthu achinyengo.
3 Kodi adzakuchitani chiyani,
ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?
4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,
ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.
5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki,
kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!
6 Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati
pa iwo amene amadana ndi mtendere.
7 Ine ndine munthu wamtendere;
koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.
Zedekiya Mfumu ya Yuda
18 Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 19 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Yehoyakimu. 20 Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake.
Kuwonongeka kwa Yerusalemu
Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.
25 Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo. 2 Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya. 3 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya. 4 Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba, 5 koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. 6 Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo. 7 Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
8 Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 9 Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika. 10 Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu. 11 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 12 Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina.
13 Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni. 14 Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo. 15 Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva.
16 Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka. 17 Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.
18 Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo. 19 Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo. 20 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula. 21 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha.
Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.
20 Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo. 21 Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu. 22 Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. 23 Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. 24 Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. 25 Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse. 26 Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa. 27 Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu. 28 Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29 Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo? 30 Ndipo kwa ife, tikuyikiranji moyo wathu pachiswe nthawi ndi nthawi? 31 Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 32 Ngati ndinalimbana ndi zirombo za kuthengo ku Efeso pa zifukwa za umunthu chabe, ndapindulanji? Ngati akufa sadzaukitsidwa,
“Tiyeni tidye ndi kumwa,
pakuti mawa tifa.”
33 Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.” 34 Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.