Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 1

BUKU LOYAMBA

Masalimo 1–41

Wodala munthu
    amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
    kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
    ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
    umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
    Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
Sizitero ndi anthu oyipa!
    Iwo ali ngati mungu
    umene umawuluzidwa ndi mphepo.
Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
    kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.

Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
    koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.

Yeremiya 13:20-27

20 Tukula maso ako kuti uwone
    amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
    nkhosa zanu zokongola zija?
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
    anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
    ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
    “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
    kuti zovala zanu zingʼambike
    ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
    kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
    zoyipa simungathe kusintha.

24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
    amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 Limeneli ndiye gawo lanu,
    chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
    ndi kutumikira milungu yabodza,
            akutero Yehova.
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
    kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
    ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
    Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
    pa zachipembedzo mpaka liti?”

1 Petro 1:17-2:1

17 Popeza mumapemphera kwa Atate amene amaweruza munthu aliyense mopanda tsankho molingana ndi zochita zake, pa nthawi imene muli alendo pa dziko lapansi khalani moopa Mulungu. 18 Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. 19 Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema. 20 Iye anasankhidwa lisanalengedwe dziko lapansi, koma waonetsedwa chifukwa cha inu pa nthawi ino yotsiriza. 21 Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa namupatsa ulemerero. Nʼchifukwa chake chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu chili mwa Mulungu.

22 Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. 23 Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24 Pakuti,

“Anthu onse ali ngati udzu,
    ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.
Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
25     koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.”

Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.

Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.