Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 138

Salimo la Davide.

138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
    ndipo ndidzayamika dzina lanu
    chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
    kupambana zinthu zonse.
Pamene ndinayitana, munandiyankha;
    munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
    pamene amva mawu a pakamwa panu.
Iwo ayimbe za njira za Yehova,
    pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
    koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
    mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
    mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
    chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
    musasiye ntchito ya manja anu.

Oweruza 3:7-11

Otanieli

Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10 Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11 Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira.

Luka 4:42-44

42 Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere. 43 Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.” 44 Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.