Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati.
56 Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri;
tsiku lonse akundithira nkhondo.
2 Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse,
ambiri akumenyana nane monyada.
3 Ndikachita mantha
ndimadalira Inu.
4 Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,
mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.
Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
5 Tsiku lonse amatembenuza mawu anga;
nthawi zonse amakonza zondivulaza.
6 Iwo amakambirana, amandibisalira,
amayangʼanitsitsa mayendedwe anga
ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.
7 Musalole konse kuti athawe;
mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
8 Mulembe za kulira kwanga,
mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu.
Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
9 Adani anga adzabwerera mʼmbuyo
pamene ndidzalirira kwa Inu.
Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
10 Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda,
mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
11 mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha.
Kodi munthu angandichite chiyani?
12 Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu;
ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
13 Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa
ndi mapazi anga kuti ndingagwe,
kuti ndiyende pamaso pa Mulungu
mʼkuwala kwa moyo.
8 Yehova anayankhula naye kuti, 9 “Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” 10 Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” 11 Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”
12 Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”
13 Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. 14 Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
15 Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. 16 Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.
Nzeru Yochokera kwa Mzimu
6 Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. 7 Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. 8 Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. 9 Komabe monga zalembedwa kuti,
“Palibe diso linaona,
palibe khutu linamva,
palibe amene anaganizira,
zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”
10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.
Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe. 11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. 12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. 13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. 14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. 15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. 16 Pakuti
“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,
kuti akhoza kumulangiza Iye.”
Koma tili nawo mtima wa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.