Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Aritasasita Atumiza Nehemiya ku Yerusalemu
2 Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. 2 Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.”
Ine ndinachita mantha kwambiri. 3 Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”
4 Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?”
Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. 5 Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”
6 Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.
7 Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. 8 Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. 9 Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane.
10 Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.
Nsembe za Moyo
12 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. 2 Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.
3 Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani. 4 Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. 5 Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake. 6 Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. 7 Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. 8 Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.