Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 36:5-10

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
    kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
    chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
    Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
    amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
    Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
    mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
    chilungamo chanu kwa olungama mtima.

Yeremiya 3:19-25

19 “Ine mwini ndinati,

“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga
    ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,
    cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’
Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’
    ndi kuti simudzaleka kunditsata.
20 Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,
    momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”
            akutero Yehova.

21 Mawu akumveka pa magomo,
    Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo
chifukwa anatsata njira zoyipa
    ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.

22 Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;
    ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.”

“Inde, tidzabwerera kwa Inu
    pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
23 Ndithu kupembedza pa magomo
    komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.
Zoonadi chipulumutso cha Israeli
    chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
24 Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu
    la ntchito za makolo athu,
nkhosa ndi ngʼombe zawo,
    ana awo aamuna ndi aakazi.
25 Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,
    ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.
Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,
    ife pamodzi ndi makolo athu
kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino
    sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”

1 Akorinto 7:1-7

Ukwati

Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire. Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa. Ndikunena zimenezi mokulolani chabe osati mokulamulani. Ine ndikanakonda anthu akanakhala ngati ine. Koma poti munthu aliyense ali ndi mphatso yakeyake yochokera kwa Mulungu, wina mphatso yake, wina yakenso.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.