Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 106:1-12

106 Tamandani Yehova.

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
    kapena kumutamanda mokwanira?
Odala ndi amene amasunga chilungamo,
    amene amachita zolungama nthawi zonse.
Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
    bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
    kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
    ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.

Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
    tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
Pamene makolo athu anali mu Igupto,
    sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
    ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
    kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
    anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
    anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo,
    palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
    ndi kuyimba nyimbo zamatamando.

Numeri 27:1-11

Ana Aakazi a Zelofehadi

27 Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.”

Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova ndipo Yehova anati kwa iye, “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.

“Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. 10 Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. 11 Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”

Luka 11:33-36

Nyale ndi Thupi

33 “Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika. 34 Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima. 35 Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima. 36 Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.