Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
106 Tamandani Yehova.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
kapena kumutamanda mokwanira?
3 Odala ndi amene amasunga chilungamo,
amene amachita zolungama nthawi zonse.
4 Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
5 kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
6 Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
7 Pamene makolo athu anali mu Igupto,
sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
8 Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
9 Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo,
palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
ndi kuyimba nyimbo zamatamando.
12 Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera;
tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.
Iwe Baraki! nyamuka
Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’
13 “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo;
anthu a Yehova anapita
kukamenyera Yehova nkhondo
kulimbana ndi adani amphamvu.
14 Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu;
akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako.
Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri,
ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
15 Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora;
inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki,
ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira.
Koma pakati pa mafuko a Rubeni
panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
16 Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera
zitoliro zoyitanira nkhosa?
Pakati pa anthu a fuko la Rubeni
panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
17 Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani.
Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi?
Aseri anali pa gombe la Nyanja;
anangokhala mʼmadooko mwawo.
18 Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa.
Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
19 “Mafumu anabwera, anachita nkhondo;
mafumu Akanaani anachita nkhondo
ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,
koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
20 Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo,
zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,
chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola.
Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
Mawu Otsiriza
13 Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha. 14 Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. 15 Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.
16 Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi. 17 Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa.
18 Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze. 19 Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo. 20 Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.
21 Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.