Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 147:12-20

12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;
    tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako
    ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako
    ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.

15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;
    mawu ake amayenda mwaliwiro.
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya
    ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
17 Amagwetsa matalala ngati miyala.
    Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;
    amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.

19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,
    malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
    anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

1 Mafumu 3:5-14

Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”

Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.

“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”

10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. 13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. 14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.”

Yohane 8:12-19

Za Umboni wa Yesu

12 Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

13 Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”

14 Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16 Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17 Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

19 Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.