Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
7 “Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa
wachira kale;
asanayambe kumva ululu,
wabala kale mwana wamwamuna.
8 Ndani anamvapo zinthu zoterezi?
Ndani anazionapo zinthu zoterezi?
Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi,
kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi?
Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa
nthawi yomweyo anabereka ana ake.
9 Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,
koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova.
“Kodi ndingatseke mimba
pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
10 “Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye,
inu nonse amene mumakonda Yerusalemu,
kondwera nayeni kwambiri,
nonse amene mumamulira.
11 Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake
ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri
wa mʼmawere
a chitonthozo chake.”
Yesu Amvera Chisoni Yerusalemu
31 Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”
32 Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.” 33 Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.
34 Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune! 35 Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.