Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
3 Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
4 Tsiku limenelo mudzati:
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
4 Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa
ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.
5 Mumanena kuti,
“Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti
kuti tigulitse zinthu?
Ndipo tsiku la Sabata litha liti
kuti tigulitse tirigu,
kuti tichepetse miyeso,
kukweza mitengo
kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
6 tigule osauka ndi ndalama zasiliva
ndi osowa powapatsa nsapato,
tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”
7 Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.
8 “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi,
ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni?
Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo;
lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata
ngati mtsinje wa ku Igupto.
9 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzadetsa dzuwa masana
ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni
ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.
Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu
ndi kumeta mipala mitu yanu.
Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,
ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
11 “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;
osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,
koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.
Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,
kufunafuna mawu a Yehova,
koma sadzawapeza.
9 Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu. 2 Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu. 3 Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera. 4 Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo. 5 Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
Kupereka Mowolowamanja
6 Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. 7 Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. 8 Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. 9 Paja analemba kuti,
“Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.”
10 Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. 11 Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.
12 Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. 13 Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense. 14 Ndipo iwowo adzakupemphererani mwachikondi chifukwa cha chisomo choposa chimene Ambuye wakupatsani. 15 Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.