Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

2 Samueli 3:31-38

31 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho. 32 Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso.

33 Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri:

“Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru.
34     Manja ako anali osamanga,
    mapazi ako anali osakulungidwa.
Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.”

Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri.

35 Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”

36 Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa. 37 Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe.

38 Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu?

Mateyu 8:18-22

Za Kutsatira Yesu

18 Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. 19 Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”

20 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”

21 Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”

22 Koma Yesu anamuwuza kuti, “Nditsate Ine ndipo uwaleke akufa ayikane akufa okhaokha.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.