Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 20

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
    dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
    akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Iye akumbukire nsembe zako zonse
    ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
            Sela
Akupatse chokhumba cha mtima wako
    ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
    ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
    Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
    ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
    koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
    koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
    Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Numeri 6:22-27

Kupereka Mdalitso

22 Yehova anawuza Mose kuti, 23 “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,

24 “ ‘Yehova akudalitse
    ndi kukusunga;
25 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
    nakuchitira chisomo;
26 Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
    nakupatse mtendere.’ ”

27 Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.

Marko 4:21-25

Fanizo la Nyale

21 Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? 22 Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. 23 Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”

24 Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. 25 Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.