Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 98

Salimo.

98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
    pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera
    zamuchitira chipulumutso.
Yehova waonetsa chipulumutso chake
    ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
Iye wakumbukira chikondi chake
    ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;
malekezero onse a dziko lapansi aona
    chipulumutso cha Mulungu wathu.

Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,
    muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,
    ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna
    fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
    dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,
    mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
izo ziyimbe pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,
    ndi mitundu ya anthu mosakondera.

Deuteronomo 32:44-47

44 Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva. 45 Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli, 46 iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa. 47 Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”

Marko 10:42-45

42 Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo. 43 Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, 44 ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. 45 Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.