Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 118:1-2

118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Israeli anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”

Masalimo 118:19-29

19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
    kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
    chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
    mwakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
    ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
    tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

25 Inu Yehova, tipulumutseni;
    Yehova, tipambanitseni.
26 Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
    Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
27 Yehova ndi Mulungu,
    ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife.
Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu,
    mpaka ku nyanga za guwa.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
    Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Deuteronomo 16:1-8

Paska

16 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.

Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.

Afilipi 2:1-11

Kutsanzira Kudzichepetsa kwa Khristu

Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:

Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,
    sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
Koma anadzichepetsa kotheratu
    nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo
    ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
Ndipo pokhala munthu choncho
    anadzichepetsa yekha
    ndipo anamvera mpaka imfa yake,
        imfa yake ya pamtanda!
Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,
    ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,
    kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye
    kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.