Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
BUKU LACHISANU
Masalimo 107–150
107 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
3 iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,
ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse
ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;
anawalanditsa ku manda.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
22 Apereke nsembe yachiyamiko
ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
5 Kenaka ine Danieli poyangʼana ndinaona anthu ena awiri atayima, wina tsidya lino la mtsinje, wina tsidya linalo. 6 Mmodzi mwa awiriwo anafunsa munthu wovala chovala chosalala amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja kuti, “Kodi padzapita nthawi yayitali bwanji kuti zodabwitsazi zidzakwaniritsidwe?”
7 Munthu wovala chovala chosalala, amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja, anakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, ndipo ndinamumva akulumbira mʼdzina la Wamoyo ku nthawi zonse uja kuti, “Zidzachitika patapita zaka zitatu ndi theka. Zinthu zonsezi zidzachitika akadzatha masautso amene agwera anthu olungama.”
8 Ndinamva, koma sindinamvetsetse. Choncho ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, nanga matsiriziro a zonsezi adzakhala chiyani?”
9 Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro. 10 Anthu ambiri adzayeretsedwa nakhala olungama wopanda chodetsa, koma oyipa adzakhala chiyipire. Palibe mmodzi wa anthu oyipa amene adzamvetsetsa koma okhawo amene ali anzeru adzamvetsetsa.
11 “Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290. 12 Wodala munthu amene adikirabe nadzafika pa mapeto a masiku 1,335.
13 “Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.”
7 Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu 8 chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso, 9 Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake. 10 Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.
11 Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, 12 nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake. 13 Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. 14 Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.