Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
111 Tamandani Yehova.
Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.
2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
malangizo ake onse ndi odalirika.
8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
9 Iyeyo amawombola anthu ake;
anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
28 Onetsetsani kuti muzimvera mawu onsewa amene ndikukupatsani kuti zinthu zizikuyenderani bwino nthawi zonse inu ndi ana anu chifukwa mudzakhala mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29 Yehova Mulungu wanu adzachotsa pamaso panu mitundu ya anthu amene mukufuna kuwathira nkhondo ndi kuwalanda dzikolo. Koma mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼdziko lawo, 30 ndipo pamene iwo awonongeka pamaso panu, samalirani kuti musakodwe mu msampha pa kufufuza za milungu yawo, nʼkumati, “Kodi anthu a mitunduwa amatumikira bwanji milungu yawo? Ifenso tichita momwemo.” 31 Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
32 Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Pergamo
12 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Pergamo kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. 13 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
14 Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo. 15 Chimodzimodzinso inuyo muli ndi ena amene amatsatira ziphunzitso za Anikolai. 16 Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.
17 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.