Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 61:1-4

Uthenga Wabwino wa Yehova

61 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,
    chifukwa Yehova wandidzoza
    kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,
    ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu
    ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;
    za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
    Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,
nkhata ya maluwa yokongola
    mʼmalo mwa phulusa,
ndiwapatse mafuta achikondwerero
    mʼmalo mwa kulira.
Ndiwapatse chovala cha matamando
    mʼmalo mwa mtima wopsinjika.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,
    yoyidzala Yehova
    kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

Adzamanganso mabwinja akale a mzinda
    ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.
Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,
    imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.

Yesaya 61:8-11

“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;
    ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.
Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika
    ndikupangana nawo pangano losatha.
Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu
    ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.
Aliyense wowaona adzazindikira
    kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”

10 Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;
    moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,
    ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.
Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,
    ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
11 Monga momwe nthaka imameretsa mbewu
    ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,
momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando
    pamaso pa mitundu yonse ya anthu.

Masalimo 126

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

126 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,
    tinali ngati amene akulota.
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;
    malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,
    “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
Yehova watichitira zinthu zazikulu,
    ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,
    monga mitsinje ya ku Negevi.
Iwo amene amafesa akulira,
    adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
Iye amene amayendayenda nalira,
    atanyamula mbewu yokafesa,
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,
    atanyamula mitolo yake.

Luka 1:46-55

Nyimbo ya Mariya

46 Ndipo Mariya anati:

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47     Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
    kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49     pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
    dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
    kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
    Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
    koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
    koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
    pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
    monga ananena kwa makolo athu.”

1 Atesalonika 5:16-24

16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20 Musanyoze mawu a uneneri. 21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.

23 Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. 24 Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.

Yohane 1:6-8

Kunabwera munthu amene anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu; Iyeyo dzina lake linali Yohane. Iye anabwera ngati mboni kudzachitira umboni kuwunikako kuti kudzera mwa iye anthu onse akhulupirire. Iyeyu sanali kuwunika; koma anabwera ngati mboni ya kuwunika.

Yohane 1:19-28

Yohane Mʼbatizi Akana kuti Iye ndi Khristu

19 Tsopano uwu ndi umboni wa Yohane pamene Ayuda a ku Yerusalemu anatumiza ansembe ndi Alevi kudzamufunsa kuti iye anali yani. 20 Iye sanalephere kuvomereza, koma iye anavomereza momasuka kuti, “Ine sindine Khristu.”

21 Iwo anamufunsa kuti, “Nanga iwe ndiwe yani? Kodi ndiwe Eliya?”

Iye anati, “Sindine.”

“Kodi ndiwe Mneneri?”

Iye anayankha kuti, “Ayi.”

22 Pomaliza iwo anati, “Ndiwe yani? Tipatse yankho kuti tipite nalo kwa amene anatituma. Kodi iwe ukuti chiyani za iwe mwini?”

23 Yohane anayankha ndi mawu a mneneri Yesaya kuti, “Ine ndi mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Wongolani njira ya Ambuye.’ ”

24 Tsopano Afarisi ena amene anatumidwa 25 anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani, umabatiza ngati iwe si Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneri?”

26 Yohane anayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panu payima amene simukumudziwa. 27 Iye ndi amene akubwera pambuyo panga, ine siwoyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”

28 Zonsezi zinachitika ku Betaniya kutsidya lina la mtsinje wa Yorodani, kumene Yohane ankabatizira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.