Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
2 Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israeli.
12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti,
“Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni,
mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”
13 Choncho dzuwa linayima,
mwezinso unayima,
mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake.
Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari.
Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu. 14 Sipanakhaleponso tsiku ngati limeneli kuyambira kale, tsiku limene Yehova anamvera munthu. Izi zinatero chifukwa Yehova ankamenyera nkhondo Aisraeli.
Miyambo ya Makolo
15 Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti, 2 “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
3 Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu? 4 Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 5 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’ 6 iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu. 7 Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
8 “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
9 Amandilambira Ine kwachabe
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.