Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 19

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
    thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
    usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
    liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
    mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
    Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
    ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
    ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
    palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

Lamulo la Yehova ndi langwiro,
    kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
    amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
    amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
    amapereka kuwala.
Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
    chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
    ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
    kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
    kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
    powasunga pali mphotho yayikulu.

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
    Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
    iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
    wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
    zikhale zokondweretsa pamaso panu,
    Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Eksodo 23:10-13

Malamulo a Nthawi Zopuma

10 “Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. 11 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.

12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.

13 “Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.

Yohane 7:40-52

40 Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”

41 Ena anati, “Iye ndiye Khristu.”

Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? 42 Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?” 43 Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. 44 Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.

Kusakhulupirira kwa Atsogoleri a Ayuda

45 Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”

46 Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”

47 Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” 48 “Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye? 49 Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”

50 Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti, 51 “Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”

52 Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.