Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 121

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
    kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Sadzalola kuti phazi lako literereke;
    Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
    sadzawodzera kapena kugona.

Yehova ndiye amene amakusunga;
    Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
    kapena mwezi nthawi ya usiku.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
    adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Eksodo 13:1-10

Mwambo Wopatula Ana Oyamba Kubadwa

13 Yehova anati kwa Mose, “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”

Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti. Pa tsiku la lero mwezi uno wa Abibu, mukutuluka mʼdziko la Igupto. Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno. Muzidzadya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri ndipo tsiku lachisanu ndi chiwirilo muzichita chikondwerero cha Yehova. Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu. Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’ Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu. 10 Muzichita mwambo uwu pa nthawi yake chaka ndi chaka.

Mateyu 21:18-22

Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu

18 Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.

20 Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”

21 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22 Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.