Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 86:1-10

Pemphero la Davide.

86 Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,
    pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.
    Inu ndinu Mulungu wanga;
    pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga.
Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,
    pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,
    pakuti ndimadalira Inu.

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,
    wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
Yehova imvani pemphero langa;
    mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,
    pakuti Inu mudzandiyankha.

Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;
    palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga
    idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;
    iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;
    Inu nokha ndiye Mulungu.

Eksodo 12:43-49

Lamulo la Paska

43 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa:

“Mlendo asadye Paska. 44 Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe. 45 Koma amene mukukhala naye kwa kanthawi kapena waganyu asadye Paska.

46 “Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse. 47 Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi.

48 “Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska. 49 Lamulo limeneli likhudza mbadwa ngakhalenso alendo wochita mdulidwe wokhala pakati panu.

Ahebri 2:5-9

Yesu Wofanana ndi Abale ake

Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,

“Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira,
    kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?
Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo;
    munamupatsa ulemerero ndi ulemu.
    Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.”

Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake. Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.