Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 33:1-12

33 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,
    nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
Mutamandeni Yehova ndi pangwe;
    muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
Muyimbireni nyimbo yatsopano;
    imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;
    Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;
    dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.

Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,
    zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;
    amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
Dziko lonse lapansi liope Yehova;
    anthu onse amulemekeze Iye.
Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;
    Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;
    Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
    zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.

Genesis 14:17-24

17 Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).

18 Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba, 19 ndipo anadalitsa Abramu nati,

“Mulungu Wammwambamwamba,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
20 Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba
    amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.”

Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.

21 Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”

22 Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira 23 kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’ 24 Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”

Machitidwe a Atumwi 28:1-10

Paulo pa Chilumba cha Melita

28 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita. Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira. Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja. Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.” Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka. Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.

Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu. Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa. Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa. 10 Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.