Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.
8 Inu Yehova Ambuye athu,
dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
mʼmayiko onse akumwamba.
2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
zimene mwaziyika pa malo ake,
4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
ndi nyama zakuthengo,
8 mbalame zamlengalenga
ndi nsomba zamʼnyanja
zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
9 Inu Yehova, Ambuye athu,
dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
Yehova Ayankhula
38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
poyankhula mawu opanda nzeru?
3 Onetsa chamuna;
ndikufunsa
ndipo undiyankhe.
4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
Ndiwuze ngati ukudziwa.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani,
kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
8 “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
8 Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu. 9 Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. 10 Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe. 11 Ine ndinasankhidwa kukhala wamthenga, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwinowu. 12 Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.