Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 37:1-17

Salimo la Davide.

37 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa
    kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,
    ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.

Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
    khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
Udzikondweretse wekha mwa Yehova
    ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Pereka njira yako kwa Yehova;
    dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,
    chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
    usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
    pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,
    usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,
    koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;
    ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko
    ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.

12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama
    ndipo amawakukutira mano;
13 koma Ambuye amaseka oyipa
    pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

14 Oyipa amasolola lupanga
    ndi kupinda uta
kugwetsa osauka ndi osowa,
    kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,
    ndipo mauta awo anathyoka.

16 Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo
    ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;
17 pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,
    koma Yehova amasunga olungama.

Rute 1:1-18

Naomi ndi Rute

Mu nthawi imene oweruza ankalamulira Israeli, munali njala mʼdziko, ndipo munthu wina wa ku Betelehemu mʼdziko la Yuda anapita pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna awiri, kukakhala ku Mowabu kwa nthawi yochepa. Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu.

Kenaka Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi anamwalira ndipo Naomiyo anatsala ndi ana ake aamuna awiri aja.

Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi, Maloni ndi Kiliyoni anamwaliranso kotero kuti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja ndi mwamuna wake.

Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kubwerera kwawo kuchokera ku Mowabu popeza anali atamva ali ku Mowabuko kuti Yehova anakomera mtima anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.

Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja anachoka kumene ankakhala ndi kuyamba ulendo obwerera kwawo ku Yuda.

Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.

“Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.

10 Ndipo anati kwa Naomi, “Ife tipita nawo kwa anthu akwanu.”

11 Koma Naomi anati, “Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu? 12 Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna, 13 kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike.”

14 Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.

15 Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.”

16 Koma Rute anayankha kuti, “Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. 17 Kumene mukafere inenso ndidzafera komweko ndipo komweko ndikayikidwa mʼmanda. Yehova andichite choyipa chingakule motani, ngati china chingatirekanitse ife kupatula imfa.”

18 Naomi atazindikira kuti Rute watsimikiza kupita naye, analeka kumukakamiza.

Filemoni

Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu.

Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu. Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.

Kuyamika ndi Pemphero

Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse. Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu. Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.

Paulo Apempha kuti Amuchitire Chifundo Onesimo

Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu, 10 ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo. 11 Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.

12 Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni. 13 Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino. 14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza. 15 Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. 16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.

17 Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo. 18 Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo. 19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo. 20 Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu. 21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.

22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.

Mawu Otsiriza

23 Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni. 24 Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.

25 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.