Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Mlandu wa Yehova ndi Israeli
6 Tamverani zimene Yehova akunena:
“Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri;
zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
2 Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri;
tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi.
Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake;
Iye akutsutsa Aisraeli.
3 “Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani?
Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
4 Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto
ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo.
Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni,
pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
5 Anthu anga, kumbukirani
zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani
ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha.
Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala,
kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
6 Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova
ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba?
Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza,
ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
7 Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000,
kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta?
Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga?
Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
8 Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino.
Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe?
Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo
ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Salimo la Davide.
15 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?
Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?
2 Munthu wa makhalidwe abwino,
amene amachita zolungama,
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,
amene sachitira choyipa mnansi wake
kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.
Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza
ngakhale pamene zikumupweteka,
5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja
ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.
Iye amene amachita zinthu zimenezi
sadzagwedezeka konse.
Khristu ndiye Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru;
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? 21 Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira. 22 Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, 23 koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. 24 Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu. 25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
26 Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. 27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. 28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, 29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu. 30 Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso. 31 Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
Chiphunzitso cha pa Phiri
5 Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye, 2 ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,
3 “Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,
chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
4 Odala ndi amene ali achisoni,
chifukwa adzatonthozedwa.
5 Odala ndi amene ali ofatsa,
chifukwa adzalandira dziko lapansi.
6 Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,
chifukwa adzakhutitsidwa.
7 Odala ndi amene ali ndi chifundo,
chifukwa adzawachitira chifundo.
8 Odala ndi amene ali oyera mtima,
chifukwa adzaona Mulungu.
9 Ndi odala amene amabweretsa mtendere,
chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,
pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
11 “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. 12 Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.