Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 27:7-14

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
    mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
    Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
Musandibisire nkhope yanu,
    musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
    mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
    Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya
    Yehova adzandisamala.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,
    munditsogolere mʼnjira yowongoka
    chifukwa cha ondizunza.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga,
    pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane
    ndipo zikundiopseza.

13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
    ndidzaona ubwino wa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
14 Dikirani pa Yehova;
    khalani anyonga ndipo limbani mtima
    nimudikire Yehova.

Oweruza 6:11-24

11 Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. 12 Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”

13 Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.”

14 Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?”

15 Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”

16 Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.”

17 Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. 18 Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.”

Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.”

19 Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.

20 Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. 21 Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. 22 Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!”

23 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.”

24 Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri.

Aefeso 5:6-14

Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.

Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti,

“Dzuka, wamtulo iwe,
    uka kwa akufa,
    ndipo Khristu adzakuwalira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.