Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 40:1-11

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

40 Mofatsa ndinadikira Yehova
    Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
    mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
    ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
    nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
    nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

Ndi wodala munthu
    amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
    kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
    ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
    palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
    zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
    koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
    Inu simunazipemphe.
Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
    Mʼbuku mwalembedwa za ine.
Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
    lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”

Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
    sinditseka milomo yanga
    monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
    ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
    pa msonkhano waukulu.

11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
    chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

Genesis 27:30-38

30 Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja. 31 Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”

32 Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?”

Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”

33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”

34 Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”

35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”

36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”

37 Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”

38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.

Machitidwe a Atumwi 1:1-5

Lonjezo la Mzimu Woyera

Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa, mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha. Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi. Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani. Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.