Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 72

Salimo la Solomoni.

72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
    Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
    anthu anu ozunzika mosakondera.
Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
    timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
    ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
    adzaphwanya ozunza anzawo.

Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
    nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
    ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
    chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
    ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
    ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
    adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
    adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
    ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
    wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
    ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
    pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

15 Iye akhale ndi moyo wautali;
    golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
    ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
    pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
    zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
    lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.

Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
    ndipo iwo adzamutcha iye wodala.

18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
    amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
    dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
            Ameni ndi Ameni.

20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.

Genesis 28:10-22

Maloto a Yakobo pa Beteli

10 Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani. 11 Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona. 12 Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo. 13 Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo. 14 Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. 15 Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”

16 Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.” 17 Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

18 Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake 19 Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi.

20 Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; 21 ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga, 22 ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”

Ahebri 11:13-22

13 Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. 14 Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. 15 Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. 16 Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.

17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. 18 Za mwana ameneyu Mulungu anamuwuza iye kuti, “Zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.” 19 Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.

20 Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau pa zatsogolo lawo.

21 Ndi chikhulupiriro, pamene Yakobo ankamwalira anadalitsa ana awiri a Yosefe, ndipo anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.

22 Ndi chikhulupiriro Yosefe ali pafupi kumwalira anayankhula za kutuluka kwa Aisraeli mu Igupto ndipo anawawuza zoti adzachite ndi mafupa ake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.