Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Pemphero la Hana
2 Ndipo Hana anapemphera nati,
“Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova;
Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova.
Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola.
Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.
2 “Palibe wina woyera ngati Yehova,
palibe wina koma inu nokha,
palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.
3 “Musandiyankhulenso modzitama,
pakamwa panu pasatuluke zonyada,
pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,
ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
4 “Mauta a anthu ankhondo athyoka
koma anthu ofowoka avala dzilimbe.
5 Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya,
koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala.
Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri,
koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.
6 “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo,
amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.
7 Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa,
amatsitsa ndipo amakweza.
8 Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi,
ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala.
Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu,
amawapatsa mpando waulemu.
“Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova,
anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
9 Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika
koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima.
“Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10 Yehova adzaphwanya omutsutsa.
Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba;
Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi.
“Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,
adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”
Kubadwa kwa Isake
21 Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. 2 Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza. 3 Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. 4 Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. 5 Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa.
6 Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” 7 Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”
Kuchotsedwa kwa Hagara ndi Ismaeli
8 Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu. 9 Koma Sara anaona kuti mwana wamwamuna amene Hagara Mwigupto anamuberekera Abrahamu amamuseka, 10 ndipo anati kwa Abrahamu, “Muchotse mdzakazi ndi mwana wake wamwamunayu, pakuti mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wanga Isake.”
11 Nkhaniyi inamumvetsa chisoni kwambiri Abrahamu chifukwa imakhudza mwana wake. 12 Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 13 Mwana wa mdzakazi wakoyu ndidzamusandutsa mtundu wa anthu chifukwa ndi mwana wako.”
14 Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.
15 Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba. 16 Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, “Sindingaonerere mwanayu akufa.” Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.
17 Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. 18 Munyamule mnyamatayo ndipo umugwire dzanja pakuti ndidzamupanga kukhala mtundu waukulu.”
19 Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe.
20 Mulungu anali ndi mnyamatayo pamene ankakula. Anakhala ku chipululu nakhala katswiri wolasa uta. 21 Akukhala ku chipululu cha Parani, mayi ake anamupezera mkazi wochokera ku Igupto.
Hagara ndi Sara
21 Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena? 22 Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu. 23 Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.
24 Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25 Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. 27 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Sangalala, iwe mayi wosabala,
amene sunabalepo mwana;
imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,
iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
kuposa mkazi wokwatiwa.”
28 Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29 Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero. 30 Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.” 31 Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.
Ufulu mwa Khristu
5 Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.