Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 2:1-10

Pemphero la Hana

Ndipo Hana anapemphera nati,

“Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova;
    Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova.
Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola.
    Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.

“Palibe wina woyera ngati Yehova,
    palibe wina koma inu nokha,
    palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

“Musandiyankhulenso modzitama,
    pakamwa panu pasatuluke zonyada,
pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,
    ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.

“Mauta a anthu ankhondo athyoka
    koma anthu ofowoka avala dzilimbe.
Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya,
    koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala.
Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri,
    koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.

“Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo,
    amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.
Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa,
    amatsitsa ndipo amakweza.
Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi,
    ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala.
Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu,
    amawapatsa mpando waulemu.

“Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova,
    anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika
    koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima.

“Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10     Yehova adzaphwanya omutsutsa.
Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba;
    Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi.

“Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,
    adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”

Genesis 17:15-22

15 Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. 16 Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”

17 Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” 18 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.”

19 Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. 20 Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. 21 Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.” 22 Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu.

Agalatiya 4:8-20

Nkhawa ya Paulo chifukwa cha Agalatiya

Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu. Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo? 10 Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka. 11 Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.

12 Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire. 13 Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka. 14 Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini. 15 Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa. 16 Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?

17 Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo. 18 Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu. 19 Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu, 20 ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.