Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 146:5-10

Wodala ndi amene thandizo lake ndi
    Mulungu wa Yakobo.
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
    nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
    Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
    ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
    Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
    Yehova amakonda anthu olungama.
Yehova amasamalira alendo
    ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
    koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
    Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.

Tamandani Yehova.

Rute 4:13-17

Makolo a Davide

13 Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna.

14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”

16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi.

17 Amayi achinansi ake anati, “Naomi ali ndi mwana wamwamuna.” Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide.

2 Petro 3:11-18

11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.

17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.