Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 2

Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
    Akonzekeranji zopanda pake anthu?
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
    ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
    ndi wodzozedwa wakeyo.
Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
    ndipo titaye zingwe zawo.”

Wokhala mmwamba akuseka;
    Ambuye akuwanyoza iwowo.
Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
    ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
    pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:

Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
    lero Ine ndakhala Atate ako.
Tandipempha,
    ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
    malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
    udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;
    chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova mwa mantha
    ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
    kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
    Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

Yeremiya 19

19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze. Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu.

“ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo. Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake. Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’

10 “Tsono iwe udzaphwanye mtsukowo anthu amene udzapite nawowo akuona, 11 ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. 12 Umu ndi mmene ndidzachitire ndi malo ano pamodzi ndi anthu okhalamo, akutero Yehova. Ndidzasandutsa mzindawu kukhala ngati Tofeti. 13 Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”

14 Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti, 15 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”

1 Timoteyo 4:6-16

Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.

Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. 10 Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.

11 Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. 13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja.

15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.