Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 104:24-34

24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
    Munazipanga zonse mwanzeru,
    dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
    yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
    zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
    ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
    kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
    zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
    izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
    izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
    zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
    izo zimalengedwa
    ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.

31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
    Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
    amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
    ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
    pamene ndikusangalala mwa Yehova.

Masalimo 104:35

35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
    ndipo anthu oyipa asapezekenso.

Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.

Tamandani Yehova.

Yesaya 44:1-4

Israeli Wosankhidwa wa Yehova

44 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Israeli, amene ndinakusankha.
Yehova
    amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
    ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Yesuruni, amene ndinakusankha.
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
    ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
    ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
    ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.

Agalatiya 6:7-10

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha. Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. 10 Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.