Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 89:1-4

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
    ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
    kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
    ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
    Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
            Sela.

Masalimo 89:19-26

19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
    kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
    ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’

Oweruza 13:2-24

Ku Zora kunali munthu wina dzina lake Manowa, wochokera ku fuko la Dani. Mkazi wake analibe ana popeza anali wosabereka. Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Tsono mudzisamale bwino, osamwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso musamadye chakudya chilichonse chodetsedwa, chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”

Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake. Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”

Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.”

Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye. 10 Tsono mkaziyo anathamanga kukawuza mwamuna wake kuti, “Wandionekeranso munthu uja amene anabwera kwa ine tsiku lija.”

11 Choncho Manowa ananyamuka namutsatira mkazi wake. Atafika kwa munthuyo anamufunsa kuti, “Kodi ndinu munayankhula ndi mkazi wanga?”

Iye anayankha kuti, “Ndine.”

12 Kenaka Manowa anafunsa kuti, “Tiyerekeze kuti mawu anuwa akwaniritsidwadi, ndiye mwanayu azidzakhala bwanji ndipo azidzachita chiyani?”

13 Ndipo mngelo wa Yehova uja anamuyankha kuti, “Zonse zimene ndinawawuza akazi anuwa asamale ndipo adzazichitedi. 14 Asadzadye chilichonse chochokera ku mphesa. Asadzamwe vinyo kapena choledzeretsa chilichonse, ngakhale kudya chakudya chilichonse chodetsedwa. Zonse zimene ndinawalamula azisunge bwino.”

15 Manowa anamuwuza mngelo wa Yehova uja kuti, “Chonde dikirani pangʼono, timati tikukonzereni mwana wambuzi.”

16 Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu).

17 Tsono Manowa anapempha mngelo wa Yehova kuti, “Chonde tidziwitseni dzina lanu kuti zikadzachitika zimene mwanenazi ife tidzakulemekezeni?”

18 Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.” 19 Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona. 20 Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi. 21 Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.

22 Iye anawuza mkazi wake kuti, “Ife tifa basi pakuti taona Mulungu!”

23 Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.”

24 Motero mkaziyo anabereka mwana wa mwamuna, namutcha dzina lake Samsoni. Iye anakula ndipo Yehova anamudalitsa.

Yohane 7:40-52

40 Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”

41 Ena anati, “Iye ndiye Khristu.”

Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? 42 Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?” 43 Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. 44 Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.

Kusakhulupirira kwa Atsogoleri a Ayuda

45 Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”

46 Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”

47 Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” 48 “Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye? 49 Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”

50 Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti, 51 “Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”

52 Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.