Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 89:1-4

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
    ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
    kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
    ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
    Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
            Sela.

Masalimo 89:19-26

19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
    kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
    ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’

2 Samueli 6:12-19

12 Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. 13 Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa. 14 Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala, 15 pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga.

16 Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake.

17 Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. 18 Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse. 19 Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake.

Ahebri 1:5-14

Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati,

“Iwe ndiwe mwana wanga;
    Ine lero ndakhala Atate ako.”

Kapena kunenanso kuti,

“Ine ndidzakhala abambo ake;
    iye adzakhala mwana wanga.”

Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati,

“Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”

Iye ponena za angelo akuti,

“Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo,
    amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”

Koma za Mwana wake akuti,

“Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya,
    ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.
Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
    Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu
    pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”

10 Mulungu akutinso,

“Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi;
    ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
11 Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire.
    Izo zidzatha ngati zovala.
12 Mudzazipindapinda ngati chofunda;
    ndipo zidzasinthidwa ngati chovala.
Koma Inu simudzasintha,
    ndipo zaka zanu sizidzatha.”

13 Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti,

“Khala kudzanja langa lamanja
    mpaka nditapanga adani ako
    kukhale chopondapo mapazi ako.”

14 Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.