Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
Yakobo Alandira Madalitso kwa Isake
27 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.”
Iye anayankha, “Ine abambo.”
2 Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa. 3 Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama. 4 Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”
5 Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama, 6 Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti, 7 ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ 8 Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: 9 Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera. 10 Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”
11 Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala. 12 Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”
13 Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”
14 Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera. 15 Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo. 16 Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi. 17 Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.
Kulimbana ndi Mphamvu za Tchimo
7 Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.” 8 Koma chifukwa cha Malamulo uchimo unapeza mwayi owutsa mʼkati mwanga khalidwe lililonse la kusirira. Pakuti pakanapanda Malamulo, uchimo ukanakhala wopanda mphamvu. 9 Nthawi ina ndinali ndi moyo popanda Malamulo. Koma nditayamba kudziwa Malamulo, pomwepo uchimo unayamba kuphuka, 10 ndipo ine ndinafa. Ine ndinazindikira kuti Malamulo omwe ankayenera kubweretsa moyo anabweretsa imfa.
11 Pakuti uchimo unapeza mwayi chifukwa cha Malamulo ndipo kudzera mʼMalamulowo, unandinyenga ndi kundiyika mu imfa. 12 Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino. 13 Kodi chomwe ndi chabwino tsopano chinasanduka imfa kwa ine? Si choncho ayi! Koma kuti uchimo uzindikirike kuti ndi uchimo unabala imfa mwa ine kudzera mu chomwe chinali chabwino, kotero kuti kudzera mu lamulo uchimo ukhale oyipa kopitirira.
14 Ife tikudziwa kuti Malamulo ndi auzimu; koma ine ndine munthu wofowoka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. 15 Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. 16 Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. 17 Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga. 18 Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita. 19 Ine sindichita zabwino zimene ndimafuna koma ndimachita zonyansa zimene sindikuzifuna. 20 Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.