Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Luka 1:46-55

Nyimbo ya Mariya

46 Ndipo Mariya anati:

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47     Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
    kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49     pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
    dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
    kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
    Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
    koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
    koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
    pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
    monga ananena kwa makolo athu.”

Mika 4:6-8

Cholinga cha Yehova

“Tsiku limenelo, Yehova akuti,

“ndidzasonkhanitsa olumala;
    ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa
    ndiponso amene ndinawalanga.
Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala.
    Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.
Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova
    kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.
Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga,
    iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni,
ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe;
    ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”

2 Petro 1:16-21

16 Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. 17 Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” 18 Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.

19 Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. 20 Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. 21 Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.