Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.
63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
kumene kulibe madzi.
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
3 Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
7 Chifukwa ndinu thandizo langa,
ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga umakangamira Inu;
dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;
adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga
ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.
15 Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera. 16 Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.
17 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?”
Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”
18 Mfumuyo inati, “Alekeni manda amenewo, munthu asachotse mafupa ake.” Choncho anawasiya mafupa akewo pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.
19 Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova. 20 Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.
21 Mfumu inalamula anthu onse kuti, “Chitani Chikondwerero cha Paska kulemekeza Yehova Mulungu wanu, motsatira zomwe zalembedwa mʼBuku la Chipangano.” 22 Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo. 23 Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, Paska imeneyi anachitira Yehova mu Yerusalemu.
24 Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova. 25 Yosiyayo asanalowe ufumu, ngakhale atamwalira, panalibenso mfumu ina yofanana naye imene inatembenukira kwa Yehova monga anachitira, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, motsatira Malamulo onse a Mose.
Mboni Ziwiri
11 Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo. 2 Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42. 3 Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” 4 Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. 5 Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo. 6 Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.
7 Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. 8 Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako. 9 Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira. 10 Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.
11 Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu. 12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.
13 Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba.
14 Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.