Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 3

Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.

Inu Yehova, achulukadi adani anga!
    Achulukadi amene andiwukira!
Ambiri akunena za ine kuti,
    “Mulungu sadzamupulumutsa.”
            Sela

Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
    Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
    ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
            Sela

Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
    ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
    abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

Dzukani, Inu Yehova!
    Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
    gululani mano a anthu oyipa.

Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
    Madalitso akhale pa anthu anu.
            Sela

1 Mafumu 8:22-30

Pemphero Lodzipereka la Solomoni

22 Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba, 23 nati:

“Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse. 24 Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu, monga mmene tikuonera lero lino.

25 “Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu, pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo mokhulupirika monga iwe wachitira.’ 26 Ndipo tsopano, Inu Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide abambo anga.

27 “Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga! 28 Koma Inu Yehova Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu lero lino. 29 Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usiku ndi usana, malo ano amene Inu munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo,’ choncho imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera akuyangʼana malo ano. 30 Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.

Marko 13:9-23

“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. 10 Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. 11 Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.

12 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 13 Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

14 “Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri. 15 Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse. 16 Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake. 17 Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! 18 Pempherani kuti zimenezi zisadzachitike nthawi yozizira, 19 chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena. 20 Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa. 21 Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. 22 Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. 23 Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.