Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 3

Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.

Inu Yehova, achulukadi adani anga!
    Achulukadi amene andiwukira!
Ambiri akunena za ine kuti,
    “Mulungu sadzamupulumutsa.”
            Sela

Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
    Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
    ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
            Sela

Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
    ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
    abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

Dzukani, Inu Yehova!
    Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
    gululani mano a anthu oyipa.

Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
    Madalitso akhale pa anthu anu.
            Sela

Deuteronomo 26:5-10

Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka. Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga. Kenaka tinafuwulira Yehova, Mulungu wa makolo athu ndipo Yehova anamva mawu athu ndi kuona kusauka, kuvutika ndi kuponderezedwa kwathu. Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa. Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. 10 Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake.

Ahebri 10:32-39

32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.

35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,

Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
    Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,
    Ine sindidzakondwera naye.

39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.