Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
4 Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. 5 Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. 6 Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa. 7 Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe. 8 Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?”
9 Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova. 10 Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. 11 Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.”
12 Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. 13 Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. 14 Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.”
15 Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. 16 Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.”
17 Eli anayankha, “Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo.”
18 Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni.
19 Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. 20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.”
Pemphero la Hana
2 Ndipo Hana anapemphera nati,
“Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova;
Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova.
Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola.
Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.
2 “Palibe wina woyera ngati Yehova,
palibe wina koma inu nokha,
palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.
3 “Musandiyankhulenso modzitama,
pakamwa panu pasatuluke zonyada,
pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,
ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
4 “Mauta a anthu ankhondo athyoka
koma anthu ofowoka avala dzilimbe.
5 Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya,
koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala.
Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri,
koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.
6 “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo,
amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.
7 Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa,
amatsitsa ndipo amakweza.
8 Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi,
ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala.
Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu,
amawapatsa mpando waulemu.
“Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova,
anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
9 Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika
koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima.
“Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10 Yehova adzaphwanya omutsutsa.
Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba;
Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi.
“Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,
adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”
11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
17 Ndipo akutinso:
“Sindidzakumbukiranso konse
machimo awo ndi zolakwa zawo.”
18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro
19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
Zizindikiro za Kutha kwa Masiku Yomaliza
13 Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”
2 Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuziona nyumba zikuluzikuluzi? Palibe mwala ndi umodzi pano umene udzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
3 Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti, 4 “Tatiwuzani, izi zidzachitika liti? Nanga chizindikiro chakuti zatsala pangʼono kukwaniritsidwa chidzakhala chiyani?”
5 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani kuti wina asakunyengeni. 6 Anthu ambiri adzabwera mʼdzina langa, nadzati, ‘Ine ndi Iyeyo,’ ndipo adzanamiza anthu ambiri. 7 Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi. 8 Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.