Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa
ndi kusagona msanga madzulo,
kuvutikira chakudya choti mudye,
pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
5 Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
18 Izi tsono ndizo zidzukulu za Perezi:
Perezi anali abambo a Hezironi.
19 Hezironi anali abambo a Ramu,
Ramu anali abambo a Aminadabu,
20 Aminadabu abambo a Naasoni,
Naasoni anali abambo a Salimoni,
21 Salimoni abambo a Bowazi,
Bowazi abambo a Obedi.
22 Obedi anali abambo a Yese,
ndipo Yese anali abambo a Davide.
Yesu Atemberera Mkuyu
12 Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. 13 Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14 Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.
Mkuyu Wofota
20 Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. 21 Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”
22 Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. 24 Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.