Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa
ndi kusagona msanga madzulo,
kuvutikira chakudya choti mudye,
pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
5 Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
11 Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu. 12 Ana amene Yehova adzakupatsa mwa mkaziyu adzamange banja lako kukhala la Perezi, amene Tamara anamubalira Yuda.”
Makolo a Davide
13 Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna.
14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”
16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi.
17 Amayi achinansi ake anati, “Naomi ali ndi mwana wamwamuna.” Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide.
15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.
16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, 17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo. 18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi. 19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse. 20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.” 21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo. 22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.
23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.