Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.
25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
kwa onse amene amathawira kwa Iye.
Rute ndi Bowazi ku Malo Wopunthira Tirigu ndi Barele
3 Tsiku lina Naomi anafunsa mpongozi wake Rute kuti, “Mwana wanga, kodi si kwabwino kuti ndikupezere kokhala kuti zinthu zizikuyendera bwino? 2 Bowazi amene adzakazi ake wakhala nawo nthawi yonseyi, si wachibale wathu kodi? Usiku uno akhala akupeta barele ku malo opunthira. 3 Samba ndi kudzola mafuta onunkhira, ndipo uvale zovala zako zabwino kwambiri. Kenaka upite ku malo opunthirako tirigu ndi barele koma munthuyo asakakuzindikire kufikira atamaliza kudya ndi kumwa. 4 Akamakagona, iwe ukaonetsetse malo amene wagonawo. Kenaka upite ndi kuvundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona. Iyeyo akakuwuza zoti uchite.”
5 Rute anayankha kuti, “Ndichita zonse zimene mwanena.”
6 Choncho Rute anapita ku malo opunthirawo ndipo anachita monga momwe apongozi ake anamuwuza.
7 Atamaliza kudya ndi kumwa, Bowazi anakhala wosangalala, ndipo anakagona pa mbali pa mulu wa barele. Tsono Rute anapita mwa kachetechete, navundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona.
17 “Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto. 18 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. 19 Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.
20 “Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu. 21 Atakamutaya, mwana wamkazi wa Farao anamutola nakamulera ngati mwana wake. 22 Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.
23 “Mose ali ndi zaka makumi anayi, anaganizira zokayendera abale ake Aisraeli. 24 Iye ataona mmodzi wa iwo akuzunzidwa ndi Mwigupto, anatchinjiriza Mwisraeliyo, namupha Mwiguptoyo. 25 Mose anaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu anamuyika kuti awapulumutse koma iwo sanazindikire. 26 Mmawa mwake Mose anaona Aisraeli awiri akukangana. Iye anayesa kuwayanjanitsa ponena kuti, ‘Amuna inu, ndinu abale; chifukwa chiyani mukufuna kupwetekana?’
27 “Koma munthu amene amavutitsa mnzakeyo anakankha Mose ndipo anati, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza. 28 Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja dzulo?’ 29 Mose atamva mawu awa anathawira ku Midiyani, kumene anakhala mlendo ndipo anabereka ana amuna awiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.