Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 146

146 Tamandani Yehova.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
    Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

Musamadalire mafumu,
    anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
    zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

Wodala ndi amene thandizo lake ndi
    Mulungu wa Yakobo.
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
    nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
    Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
    ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
    Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
    Yehova amakonda anthu olungama.
Yehova amasamalira alendo
    ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
    koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
    Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.

Tamandani Yehova.

Rute 1:18-22

18 Naomi atazindikira kuti Rute watsimikiza kupita naye, analeka kumukakamiza.

19 Choncho amayi awiriwo anapitiriza ulendo wawo mpaka anakafika ku Betelehemu. Pamene ankafika mu Betelehemu, anthu onse a mʼmudzimo anatekeseka chifukwa cha iwowo ndipo amayi ambiri ankanena kuti, “Kodi uyu nʼkukhala Naomi?”

20 Iye anawawuza kuti, “Musanditchenso Naomi. Muzinditchula ine kuti Mara, chifukwa Wamphamvuzonse wandizunza kwambiri. 21 Ine ndinapita wolemera, koma Yehova wabwera nane wopanda kanthu. Nanga munditchulirenji Naomi pamene Yehova wandisautsa. Wamphamvuzonse uja wandigwetsera mavuto owawa.”

22 Naomi anabwerera kuchoka ku dziko la Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake. Ndipo anafika ku Betelehemu nthawi yoyamba kukolola barele.

Ahebri 9:1-12

Kupembedza mʼTenti ya Dziko Lapansi

Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika. Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri. Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.

Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo. Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira. Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo. Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo. 10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.

Magazi a Yesu

11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.