Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 28

Salimo la Davide.

28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
    musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
    ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Imvani kupempha chifundo kwanga
    pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
    kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
    pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
    koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
    ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
    ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
    ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
    ndipo sadzawathandizanso.

Matamando apite kwa Yehova,
    popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
    mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
    ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
    linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
    mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.

Ezekieli 14:12-23

Chilango Chosathawika

12 Yehova anayankhula nane kuti, 13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 14 Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

15 “Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo. 16 Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’

17 “Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 18 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’

19 “Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 20 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.

21 “Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe! 22 Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu. 23 Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”

Mateyu 20:29-34

Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona

29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”

33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”

34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.